Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:41

[1] Yehova akulamulira, mitundu ya anthu injenjemere; Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi, dziko lapansi ligwedezeke.

[2] Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova; Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.

[3] Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri, Iye ndi woyera.

[4] Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera; mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.

[5] Kwezani Yehova Mulungu wathu ndipo mulambireni pa mapazi ake; Iye ndi woyera.

[6] Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake, Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake; iwo anayitana Yehova ndipo Iyeyo anawayankha.

[7] Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo; iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.

[8] Inu Yehova Mulungu wathu, munawayankha iwo; Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka, ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa.

[9] Kwezani Yehova Mulungu wathu ndipo mumulambire pa phiri lake loyera, pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.

Masalimo — Chapters