Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:05

[1] Mundichitire chifundo, Inu Mulungu mundichitire chifundo, pakuti mwa Inu moyo wanga umathawiramo. Ndidzathawira mu mthunzi wa mapiko anu mpaka chiwonongeko chitapita.

[2] Ine ndikufuwulira kwa Mulungu Wammwambamwamba, kwa Mulungu amene amakwaniritsa cholinga chake pa ine.

[3] Mulungu amanditumizira kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa, kudzudzula iwo amene akundithamangitsa kwambiri. Mulungu amatumiza chikondi chake ndi kukhulupirika kwake.

[4] Ine ndili pakati pa mikango, ndagona pakati pa zirombo zolusa; anthu amene mano awo ndi milomo yawo ndi mivi, malilime awo ndi malupanga akuthwa.

[5] Mukwezekedwe Inu Mulungu, kuposa mayiko onse akumwamba; mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.

[6] Iwo anatchera mapazi anga ukonde ndipo ndinawerama pansi mosautsidwa. Anakumba dzenje mʼnjira yanga koma agweramo okha mʼmenemo.

[7] Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu mtima wanga ndi wokhazikika. Ndidzayimba nyimbo, nyimbo yake yamatamando.

[8] Dzuka moyo wanga! Dzukani zeze ndi pangwe! Ndidzadzuka mʼbandakucha.

[9] Ndidzakutamandani Ambuye, pakati pa mitundu ya anthu, ndidzayimba za Inu pakati pa mayiko.

[10] Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kufikira ku mayiko akumwamba; kukhulupirika kwanu kwafika ku mitambo.

[11] Mukwezekedwe Inu Mulungu kuposa mayiko akumwamba, mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.

Masalimo — Chapters