Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 0:50

[1] Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi.

[2] Mulambireni Yehova mosangalala; bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero.

[3] Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu. Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.

[4] Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko ndi ku mabwalo ake ndi matamando; muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.

[5] Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya; kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.

Masalimo — Chapters