Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:24

[1] Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.

[2] Ndidzanena za Yehova, “Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa, Mulungu wanga amene ndimadalira.”

[3] Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa mlenje ndi ku mliri woopsa;

[4] Adzakuphimba ndi nthenga zake, ndipo udzapeza malo othawira mʼmapikomo; kukhulupirika kwake kudzakhala chishango chako ndi lihawo.

[5] Sudzachita mantha ndi zoopsa za usiku, kapena muvi wowuluka masana,

[6] kapena mliri umene umayenda mu mdima, kapena zowononga za pa nthawi ya masana.

[7] Anthu 1,000 atha kufa pambali pako, anthu 10,000 kudzanja lako lamanja, koma zoopsazo sizidzafika pafupi ndi iwe.

[8] Udzapenya ndi maso ako ndipo udzaona mmene anthu oyipa amalangidwira.

[9] Pakuti wasankha Wammwambamwamba kukhala malo ako okhalamo; wavomera Yehova kukhala kothawira kwako.

[10] Choncho palibe choyipa chimene chidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi tenti yako.

[11] Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, kuti akutchinjirize mosamala pa njira zako zonse;

[12] ndipo adzakunyamula ndi manja awo, kuti phazi lako lisagunde pa mwala.

[13] Udzapondaponda mkango ndi njoka, udzapondereza mkango wamphamvu ndiponso chinjoka.

[14] “Chifukwa iye amandikonda,” akutero Yehova, “Ndidzamulanditsa; ndidzamuteteza pakuti wavomereza dzina langa.

[15] Adzandiyitana, ndipo ndidzamuyankha; ndidzakhala naye pa mavuto, ndidzamupulumutsa ndi kumulemekeza.

[16] Ndidzamupatsa moyo wautali ndi kumupulumutsa.”

Masalimo — Chapters