Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:07

[1] Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri; mwavala ulemerero ndi ufumu.

[2] Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala; watambasula miyamba ngati tenti

[3] ndipo wayika pa madzi mitanda ya chipinda chake. Iye amasandutsa mitambo kukhala galeta lake, ndi kuwuluka pa mapiko a mphepo.

[4] Amapanga mphepo kukhala amithenga ake, malawi amoto kukhala atumiki ake.

[5] Anakhazikitsa dziko lapansi pa maziko ake; silingasunthike.

[6] Munaliphimba ndi nyanja yozama ngati chovala; madzi anayimirira pamwamba pa mapiri.

[7] Koma pakudzudzula kwanu madzi anathawa, pa mkokomo wa bingu lanu iwo anamwazika;

[8] Inu munamiza mapiri, iwo anatsikira ku zigwa kumalo kumene munawakonzera.

[9] Inu munayika malire ndipo sangathe kudutsa, iwo sadzamizanso dziko lapansi.

[10] Iye achititsa akasupe kutulutsa madzi kupita ku zigwa; madziwo amayenda pakati pa mapiri.

[11] Iwo amapereka madzi kwa zirombo zonse zakuthengo; abulu akuthengo amapha ludzu lawo.

[12] Mbalame zamlengalenga zimayika zisa mʼmbali mwa madzi; zimayimba pakati pa thambo.

[13] Iye amathirira mapiri kuchokera ku zipinda zake zapamwamba; dziko lapansi limakhutitsidwa ndi chipatso cha ntchito yake.

[14] Amameretsa udzu kuti ngʼombe zidye, ndi zomera, kuti munthu azilima kubweretsa chakudya kuchokera mʼdziko lapansi:

[15] vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu, mafuta amene amachititsa nkhope yake kuwala, ndi buledi amene amapereka mphamvu.

[16] Mitengo ya Yehova ndi yothiriridwa bwino, mikungudza ya ku Lebanoni imene Iye anadzala.

[17] Mbalame zimamanga zisa zawo; kakowa ali ndi malo ake mʼmikungudzamo.

[18] Mapiri ataliatali ndi a mbalale; mʼmingʼalu ya miyala ndi mobisalamo mbira.

[19] Mwezi umasiyanitsa nyengo ndipo dzuwa limadziwa nthawi yake yolowera.

[20] Inu mumabweretsa mdima nukhala usiku, ndipo zirombo zonse za ku nkhalango zimatuluka.

[21] Mikango imabangula kufuna nyama, ndi kufunafuna chakudya chawo kuchokera kwa Mulungu.

[22] Dzuwa limatuluka ndipo iyo imapita kukabisala; imabwerera kukagona pansi mʼmapanga awo.

[23] Pamenepo munthu amapita ku ntchito yake, kukagwira ntchito yake mpaka madzulo.

[24] Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova! Munazipanga zonse mwanzeru, dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.

[25] Kuli nyanja yayikulu ndi yotambalala, yodzaza ndi zolengedwa zosawerengeka, zamoyo zanu zazikulu ndi zazingʼono zomwe.

[26] Kumeneko sitima zapamadzi zimayenda uku ndi uku, ndiponso Leviyatani amene munamulenga kuti asewere kumeneko.

[27] Zonsezi zimayangʼana kwa Inu kuti muzipatse chakudya chawo pa nthawi yake yoyenera.

[28] Mukazipatsa, zimachisonkhanitsa pamodzi; mukatsekula dzanja lanu, izo zimakhutitsidwa ndi zinthu zabwino.

[29] Mukabisa nkhope yanu, izo zimachita mantha aakulu; mukachotsa mpweya wawo, zimafa ndi kubwerera ku fumbi.

[30] Mukatumiza mzimu wanu, izo zimalengedwa ndipo mumakozanso maonekedwe a dziko lapansi.

[31] Ulemerero wa Yehova ukhalebe mpaka muyaya; Yehova akondwere ndi ntchito ya manja ake;

[32] Iye amene amayangʼana dziko lapansi ndipo limanjenjemera, amene amakhudza mapiri ndipo amatuluka utsi.

[33] Ine ndidzayimbira Yehova moyo wanga wonse; ndidzayimbira matamando Mulungu wanga nthawi yonse imene ndili ndi moyo.

[34] Zolingalira zanga zikhale zomukomera Iye, pamene ndikusangalala mwa Yehova.

[35] Koma anthu ochimwa awonongeke pa dziko lapansi ndipo anthu oyipa asapezekenso. Tamanda Yehova, Iwe moyo wanga. Tamandani Yehova.

Masalimo — Chapters