Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:02

[1] Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu; Iye akuweruza pakati pa “milungu.”

[2] “Mudzateteza osalungama mpaka liti, ndi kukondera anthu oyipa?

[3] Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye; mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika.

[4] Landitsani anthu ofowoka ndi osowa; apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.

[5] “Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse. Amayendayenda mu mdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.

[6] “Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu, nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’

[7] Koma mudzafa ngati anthu wamba; mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.”

[8] Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi, pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.

Masalimo — Chapters