Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:57

[1] Kodi inu olamulira mumayankhuladi molungama? Kodi mumaweruza mwachilungamo pakati pa anthu?

[2] Ayi, mʼmitima mwanu mumakonzekera zosalungama, ndipo manja anu amatulutsa zachiwawa pa dziko lapansi.

[3] Ngakhale kuchokera tsiku lawo lobadwa oyipa amasochera; kuchokera mʼmimba ya amayi awo, iwo ndi otayika ndipo amayankhula mabodza.

[4] Ululu wawo uli ngati ululu wa njoka, ngati uja wa mphiri imene yatseka mʼmakutu mwake.

[5] Imene simva liwu la munthu wamatsenga, ngakhale akhale wa luso lotani munthu wamatsengayo.

[6] Gululani mano mʼkamwa mwawo, Inu Mulungu, Yehova khadzulani mano a mikango!

[7] Mulole kuti asowe ngati madzi oyenda pamene iwo akoka uta mulole kuti mivi yawo ikhale yosathwa.

[8] Akhale ngati nkhono imene imasungunuka pamene ikuyenda; ngati mwana wakufa asanabadwe, iwo asaone dzuwa.

[9] Miphika yanu isanagwire moto waminga ya mkandankhuku, kaya iyo ndi yobiriwira kapena yowuma, oyipa adzachotsedwa.

[10] Olungama adzasangalala poona kubwezera chilango, pamene adzasambitsa mapazi awo mʼmagazi a anthu oyipa.

[11] Ndipo anthu adzanena kuti, “Zoonadi, olungama amalandirabe mphotho; zoonadi kuli Mulungu amene amaweruza dziko lapansi.”

Masalimo — Chapters