Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:58

[1] Mwa Inu Yehova ine ndathawiramo; musalole kuti ndichititsidwe manyazi.

[2] Mundilanditse ndi kundipulumutsa mwa chilungamo chanu, mutchere khutu lanu ndi kundipulumutsa.

[3] Mukhale thanthwe langa lothawirapo, kumene ine nditha kupita nthawi zonse; lamulani kuti ndipulumuke, pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.

[4] Landitseni Inu Mulungu wanga, kuchoka mʼdzanja la oyipa, kuchoka mʼdzanja la oyipa ndi anthu ankhanza.

[5] Pakuti Inu mwakhala chiyembekezo changa, Inu Ambuye Wamphamvuzonse, chilimbikitso changa kuyambira ndili mwana.

[6] Kuyambira pamene ndinabadwa, ndakhala ndikudalira Inu; Inu munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga, ndipo ndidzakupembedzani nthawi zonse.

[7] Ine ndakhala chinthu chodabwitsa kwa anthu ambiri koma Inu ndinu wonditchinjiriza wamphamvu.

[8] Pakamwa panga padzaza ndi matamando anu, kulengeza ulemerero wanu tsiku lonse.

[9] Musanditaye pamene ndakalamba; musandisiye pamene mphamvu zanga zatha.

[10] Pakuti adani anga ayankhula motsutsana nane; iwo amene amadikira kuti andiphe amapangana pamodzi.

[11] Iwo amati, “Mulungu wamusiya; mutsatireni ndi kumugwira, pakuti palibe amene adzamupulumutse.”

[12] Musakhale kutali ndi ine Inu Mulungu, bwerani msanga, Inu Mulungu wanga; thandizeni.

[13] Ondineneza anga awonongeke mwa manyazi, iwo amene akufuna kundipweteka avale chitonzo ndi manyazi.

[14] Koma ine ndidzakhala ndi chiyembekezo mwa Inu nthawi zonse, ndidzakutamandani mowirikizawirikiza.

[15] Pakamwa panga padzafotokoza za chilungamo chanu, za chipulumutso chanu tsiku lonse, ngakhale sindikudziwa muyeso wake.

[16] Ndidzabwera ndi kulengeza za machitidwe amphamvu zanu Inu Ambuye Wamphamvuzonse. Ndidzalengeza chilungamo chanu, chanu chokha.

[17] Kuyambira ubwana wanga, Inu Mulungu mwakhala mukundiphunzitsa, ndipo mpaka lero ine ndikulengeza za ntchito zanu zodabwitsa

[18] Ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbuu musanditaye Inu Mulungu, mpaka nditalengeza mphamvu zanu kwa mibado yonse yakutsogolo.

[19] Mphamvu zanu ndi kulungama kwanu zimafika mpaka kumwambamwamba. Ndani wofanana nanu Inu Mulungu, amene mwachita zazikulu?

[20] Ngakhale mwandionetsa mavuto ambiri owawa, mudzabwezeretsanso moyo wanga; kuchokera kunsi kwa dziko lapansi, mudzandiukitsanso.

[21] Inu mudzachulukitsa ulemu wanga ndi kunditonthozanso.

[22] Ndidzakutamandani ndi zeze chifukwa cha kukhulupirika kwanu Mulungu, ndidzayimba matamando kwa Inu ndi pangwe, Inu Woyera wa Israeli.

[23] Milomo yanga idzafuwula ndi chimwemwe pamene ndidzayimba matamando kwa Inu amene mwandiwombola.

[24] Lilime langa lidzafotokoza za ntchito zanu zachilungamo tsiku lonse, pakuti iwo amene amafuna kundipweteka achititsidwa manyazi ndi kusokonezedwa.

Masalimo — Chapters