Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:40

[1] Yehova musandidzudzule mutapsa mtima kapena kundilanga muli ndi ukali.

[2] Pakuti mivi yanu yandilasa, ndipo dzanja lanu latsika ndipo landifikira.

[3] Chifukwa cha ukali wanu mulibe thanzi mʼthupi langa; mafupa anga alibe mphamvu chifukwa cha tchimo langa.

[4] Kulakwa kwanga kwandipsinja ngati katundu wolemera kwambiri kuposa mphamvu zanga.

[5] Mabala anga akuwola ndipo akununkha chifukwa cha uchitsiru wa moyo wanga wauchimo.

[6] Ine ndapindika msana ndipo ndawerama kwambiri; tsiku lonse ndimangolira.

[7] Msana wanga wagwidwa ndi ululu wosasimbika, mulibe thanzi mʼthupi langa.

[8] Ndilibe mphamvu ndipo ndakunthidwa kwathunthu; ndikubuwula ndi ululu wa mumtima.

[9] Zokhumba zanga zonse zili poonekera pamaso panu Ambuye, kusisima kwanga sikunabisike kwa Inu.

[10] Mtima wanga ukugunda, mphamvu zanga zikutha; ngakhale kuwala kwachoka mʼmaso mwanga.

[11] Abwenzi anga ndi anzanga akundipewa chifukwa cha mabala anga; anansi anga akhala kutali nane.

[12] Iwo amene akufunafuna moyo wanga atchera misampha yawo, oti andipwetekewo amayankhula za kuwonongeka kwanga; tsiku lonse amakonza zachinyengo.

[13] Ine ndili ngati munthu wosamva amene sangamve, monga wosayankhula, amene sangathe kutsekula pakamwa pake;

[14] Ndakhala ngati munthu amene samva, amene pakamwa pake sipangathe kuyankha.

[15] Ndikudikira Inu Yehova; mudzayankha, Inu Ambuye Mulungu wanga.

[16] Pakuti Ine ndinati, “Musawalole kuti akondwere kapena kudzikweza okha pa ine pamene phazi langa laterereka.”

[17] Pakuti ndili pafupi kugwa, ndipo ndikumva kuwawa nthawi zonse.

[18] Ndikuvomereza mphulupulu zanga; ndipo ndavutika ndi tchimo langa.

[19] Ambiri ndi adani anga amphamvu; amene amandida popanda chifukwa alipo ochuluka kwambiri.

[20] Iwo amene amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino amandinyoza pamene nditsatira zabwino.

[21] Inu Yehova, musanditaye; musakhale kutali ndi ine Mulungu wanga.

[22] Bwerani msanga kudzandithandiza, Inu Ambuye Mpulumutsi wanga.

Masalimo — Chapters