Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 0:57

[1] Yehova akapanda kumanga nyumba, omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe. Yehova akapanda kulondera mzinda, mlonda akanangolondera pachabe.

[2] Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa ndi kusagona msanga madzulo, kuvutikira chakudya choti mudye, pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.

[3] Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova, ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.

[4] Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja mwa munthu wankhondo.

[5] Wodala munthu amene motengera mivi mwake mwadzaza. Iwo sadzachititsidwa manyazi pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.

Masalimo — Chapters