Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:14

[1] Mofatsa ndinadikira Yehova Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.

[2] Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko, mʼthope ndi mʼchithaphwi; Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwe ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba.

[3] Iye anayika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga, nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga. Ambiri adzaona, nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova.

[4] Ndi wodala munthu amakhulupirira Yehova; amene sayembekezera kwa odzikuza, kapena kwa amene amatembenukira kwa milungu yabodza.

[5] Zambiri, Yehova Mulungu wanga, ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita. Zinthu zimene munazikonzera ife palibe amene angathe kukuwerengerani. Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera, zidzakhala zambiri kuzifotokoza.

[6] Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna, koma makutu anga mwawatsekula; zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimo Inu simunazipemphe.

[7] Kotero ndinati, “Ndili pano, ndabwera. Mʼbuku mwalembedwa za ine.

[8] Ndikufuna kuchita chifuniro chanu, Inu Mulungu wanga; lamulo lanu lili mu mtima mwanga.”

[9] Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu; sinditseka milomo yanga monga mukudziwa Inu Yehova.

[10] Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga; ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu. Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu pa msonkhano waukulu.

[11] Musandichotsere chifundo chanu Yehova; chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.

[12] Pakuti mavuto osawerengeka andizungulira; machimo anga andigonjetsa, ndipo sindingathe kuona. Alipo ambiri kuposa tsitsi la mʼmutu mwanga, ndipo mtima wanga ukufowoka mʼkati mwanga.

[13] Pulumutseni Yehova; Bwerani msanga Yehova kudzandithandiza.

[14] Onse amene akufunafuna kuchotsa moyo wanga achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa; onse amene amakhumba chiwonongeko changa abwezedwe mwamanyazi.

[15] Iwo amene amanena kwa ine kuti, “Hee! Hee!” abwerere akuchita manyazi.

[16] Koma iwo amene amafunafuna Inu akondwere ndi kusangalala mwa Inu; iwo amene amakonda chipulumutso chanu nthawi zonse anene kuti, “Yehova akwezeke!”

[17] Komabe Ine ndine wosauka ndi wosowa; Ambuye andiganizire. Inu ndinu thandizo langa ndi wondiwombola wanga; Inu Mulungu wanga, musachedwe.

Masalimo — Chapters