Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:35

[1] Tamandani Yehova. Wodala munthu amene amaopa Yehova, amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake.

[2] Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko; mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa.

[3] Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake, ndipo chilungamo chake ndi chosatha.

[4] Ngakhale mu mdima kuwala kumatulukira olungama mtima; wokoma mtima, wachifundo ndi wowongoka mtima.

[5] Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu, amene amachita ntchito yake mwachilungamo.

[6] Ndithu sadzagwedezeka; munthu wolungama sadzayiwalika mpaka muyaya.

[7] Saopa akamva zoyipa zimene zachitika; mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova.

[8] Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha; potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano.

[9] Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, chilungamo chake chimanka mpaka muyaya; nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu.

[10] Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima; adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka. Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.

Masalimo — Chapters