Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:07

[1] Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu; ndidzayimba nyimbo, inde ndidzayimba nyimbo zotamanda ndi moyo wanga wonse.

[2] Dzukani, zeze ndi pangwe! Ine ndidzadzutsa mʼbandakucha.

[3] Ndidzakutamandani Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina; ndidzayimba za Inu pakati pa anthu a mitundu ina.

[4] Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kutalika kwake kuposa kumwamba; kukhulupirika kwanu kumafika mlengalenga.

[5] Kwezekani Inu Mulungu, kuposa mayiko akumwamba, ndipo ulemerero wanu uphimbe dziko lonse lapansi.

[6] Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.

[7] Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika: “Mwachipambano Ine ndidzagawa Sekemu ndipo ndidzayesa chigwa cha Sukoti.

[8] Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso; Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera, Yuda ndi ndodo yanga yaufumu.

[9] Mowabu ndi mbale yanga yosambiramo ndidzaponya nsapato zanga pa Edomu; ndidzafuwula mopambana pa Filisitiya.”

[10] Ndani adzandifikitsa ku mzinda wotetezedwa? Ndani adzanditsogolera ku Edomu?

[11] Kodi sindinu Mulungu, Inu amene mwatikana ndipo simuperekezanso magulu athu ankhondo?

[12] Tithandizeni ife kulimbana ndi mdani, pakuti thandizo la munthu ndi lopanda pake.

[13] Chifukwa cha Mulungu wathu, ife tidzapeza chipambano, ndipo adzapondereza pansi adani athu.

Masalimo — Chapters