Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:35

[1] Tikuthokoza Inu Mulungu, tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe, anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.

[2] Mumati, “Ine ndimayika nthawi yoyenera, ndine amene ndimaweruza mwachilungamo.

[3] Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera, ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba. q4 Sela

[4] Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’ ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.

[5] Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba; musayankhule ndi khosi losololoka.’ ”

[6] Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo kapena ku chipululu.

[7] Koma ndi Mulungu amene amaweruza: Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.

[8] Mʼdzanja la Yehova muli chikho chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera; Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi amamwa ndi senga zake zonse.

[9] Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya; ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo.

[10] Ndidzadula nyanga za onse oyipa koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.

Masalimo — Chapters