Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:28

[1] Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama; kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando.

[2] Ndidzatsata njira yolungama; nanga mudzabwera liti kwa ine? Ndidzayenda mʼnyumba mwanga ndi mtima wosalakwa.

[3] Sindidzayika chinthu chilichonse choyipa pamaso panga. Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro; iwo sadzadziphatika kwa ine.

[4] Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine; ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine.

[5] Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri ameneyo ndidzamuletsa; aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza, ameneyo sindidzamulekerera.

[6] Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko, kuti akhale pamodzi ndi ine; iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa adzanditumikira.

[7] Aliyense wochita chinyengo sadzakhala mʼnyumba mwanga. Aliyense woyankhula mwachinyengo sadzayima pamaso panga.

[8] Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthu onse oyipa mʼdziko; ndidzachotsa aliyense wochita zoyipa mu mzinda wa Yehova.

Masalimo — Chapters