Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:08

[1] Moyo wanga umapeza mpumulo mwa Mulungu yekha; chipulumutso changa chimachokera kwa Iye.

[2] Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka.

[3] Kodi nonsenu mudzalimbana naye munthu mpaka liti? Kodi mudzamugwetsa pansi ngati khoma losalimba, ngati mpanda wogwedezeka?

[4] Iwo akufunitsitsa kumugwetsa kuti achoke pa malo ake apamwamba. Iwo amakondweretsedwa ndi mabodza. Ndi pakamwa pawo amadalitsa koma mʼmitima yawo amatemberera.

[5] Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga; chiyembekezo changa chichokera mwa Iye.

[6] Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; Iyeyo ndi linga langa; sindidzagwedezeka.

[7] Chipulumutso changa ndi ulemu wanga zimachokera kwa Mulungu: Iye ndiye thanthwe langa lamphamvu; Mulungu ndiye pothawira panga.

[8] Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu; khuthulani mitima yanu kwa Iye, pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu. q4 Sela

[9] Anthu wamba ndi mpweya chabe; anthu apamwamba ndi bodza chabe; ngati atayezedwa pa sikelo iwo ndi chabe; iwowo pamodzi ndi mpweya ndi chabe

[10] Musadalire kulanda mwachinyengo kapena katundu wobedwa; ngakhale chuma chanu chichuluke, musayike mtima wanu pa icho.

[11] Mulungu wayankhula kamodzi, ine ndamvapo zinthu ziwiri; choyamba nʼchakuti Inu Mulungu ndinu wamphamvu,

[12] komanso Inu Ambuye, chikondi chanu nʼchosasinthika. Chachiwiri nʼchakuti mumamuchitira munthu molingana ndi ntchito zake.

Masalimo — Chapters