[1] Inu Yehova, kumbukirani Davide ndi mavuto onse anapirira.
[2] Iye analumbira kwa Yehova ndi kulonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti,
[3] “Sindidzalowa mʼnyumba mwanga kapena kugona pa bedi langa:
[4] sindidzalola kuti maso anga agone, kapena zikope zanga ziwodzere,
[5] mpaka nditamupezera malo Yehova, malo okhala a Wamphamvu wa Yakobo.”
[6] Zoonadi, tinamva za Bokosi la Chipangano ku Efurata, tinalipeza mʼminda ya ku Yaara:
[7] “Tiyeni tipite ku malo ake okhalamo; tiyeni tikamulambire pa mapazi ake.
[8] ‘Dzukani Yehova, ndipo bwerani ku malo anu opumulira, Inuyo ndi Bokosi la Chipangano limene limafanizira mphamvu zanu.
[9] Ansembe anu avekedwe chilungamo; anthu anu oyera mtima ayimbe nyimbo mwachimwemwe.’ ”
[10] Chifukwa cha Davide mtumiki wanu, musakane wodzozedwa wanu.
[11] Yehova analumbira kwa Davide, lumbiro lotsimikizika kuti Iye sadzasintha: “Mmodzi wa ana ako ndidzamuyika pa mpando waufumu;
[12] ngati ana ako azisunga pangano langa ndi malamulo amene ndiwaphunzitsa, pamenepo ana awo adzakhala pa mpando wako waufumu kwamuyaya ndi muyaya.”
[13] Pakuti Yehova wasankha Ziyoni, Iye wakhumba kuti akhale malo ake okhalamo:
[14] “Awa ndi malo anga opumapo ku nthawi za nthawi; ndidzakhala pano pa mpando waufumu, pakuti ndakhumba zimenezi.
[15] Ndidzadalitsa mzindawu ndi zinthu zambiri; anthu ake osauka ndidzawakhutitsa ndi chakudya.
[16] Ndidzaveka ansembe ake chipulumutso, ndipo anthu ake oyera mtima adzayimba nthawi zonse nyimbo zachimwemwe.
[17] “Pano ndidzachulukitsa mphamvu za Davide ndi kuyikapo nyale ya wodzozedwa wanga.
[18] Ndidzaveka adani ake manyazi, koma chipewa chaufumu pamutu pake chidzakhala chowala.”