Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 0:58

[1] “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,” anene tsono Israeli;

[2] “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga, koma sanandipambane.

[3] Anthu otipula analima pa msana panga ndipo anapangapo mizere yayitali:

[4] Koma Yehova ndi wolungama; Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.”

[5] Onse amene amadana ndi Ziyoni abwezedwe pambuyo mwamanyazi.

[6] Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba, umene umafota usanakule;

[7] sungadzaze manja a owumweta kapena manja a omanga mitolo.

[8] Odutsa pafupi asanene kuti, “Dalitso la Yehova lili pa inu; tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”

Masalimo — Chapters