Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:27

[1] Inu Yehova, mwandisanthula ndipo mukundidziwa.

[2] Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka; mumazindikira maganizo anga muli kutali.

[3] Mumapenyetsetsa pamene ndikutuluka ndi kugona kwanga; mumadziwa njira zanga zonse.

[4] Mawu asanatuluke pa lilime langa mumawadziwa bwinobwino, Inu Yehova.

[5] Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo komwe; mwasanjika dzanja lanu pa ine.

[6] Nzeru zimenezi ndi zopitirira nzeru zanga, ndi zapamwamba kuti ine ndizipeze.

[7] Kodi ndingapite kuti kufuna kuzemba Mzimu wanu? Kodi ndingathawire kuti kuchoka pamaso panu?

[8] Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko; ndikakagona ku malo a anthu akufa, Inu muli komweko.

[9] Ngati ndiwulukira kotulukira dzuwa, ngati ndikakhala ku malekezero a nyanja,

[10] kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandigwiriziza.

[11] Ndikanena kuti, “Zoonadi, mdima udzandibisa ndithu ndipo kuwunika kukhale mdima mondizungulira,”

[12] komabe mdimawo sudzakhala mdima kwa Inu; usiku udzawala ngati masana, pakuti mdima uli ngati kuwunika kwa Inu.

[13] Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga; munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.

[14] Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa; ntchito zanu ndi zodabwitsa, zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.

[15] Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi, pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.

[16] Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe. Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.

[17] Zolingalira zanu pa ine ndi zamtengowapatali, Inu Mulungu, ndi zosawerengeka ndithu!

[18] Ndikanaziwerenga, zikanakhala zochuluka kuposa mchenga; pamene ndadzuka, ndili nanube.

[19] Ndi bwino mukanangopha anthu oyipa, Inu Mulungu! Chokereni inu anthu owononga anzanu!

[20] Amayankhula za Inu ndi zolinga zoyipa; adani anu amagwiritsa ntchito dzina lanu molakwika.

[21] Kodi ine sindidana nawo amene amakudani, Inu Yehova? Kodi sindinyansidwa nawo amene amakuwukirani?

[22] Ndimadana nawo kwathunthu; ndi adani anga.

[23] Santhuleni, Inu Mulungu ndipo mudziwe mtima wanga; Yeseni ndipo mudziwe zolingalira zanga.

[24] Onani ngati muli mayendedwe aliwonse oyipa mwa ine, ndipo munditsogolere mʼnjira yanu yamuyaya.

Masalimo — Chapters