[1] Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa; mvetserani mawu a pakamwa panga.
[2] Ndidzatsekula pakamwa panga mʼmafanizo, ndidzayankhula zinthu zobisika, zinthu zakalekale
[3] zimene tinazimva ndi kuzidziwa, zimene makolo athu anatiwuza.
[4] Sitidzabisira ana awo, tidzafotokozera mʼbado wotsatira ntchito zotamandika za Yehova, mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.
[5] Iye anapereka mawu wodzichitira umboni kwa Yakobo ndi kukhazikitsa lamulo mu Israeli, zimene analamulira makolo athu kuphunzitsa ana awo,
[6] kotero kuti mʼbado wotsatira uthe kuzidziwa, ngakhale ana amene sanabadwe, ndi kuti iwo akafotokozere ana awonso.
[7] Choncho iwo adzakhulupirira Mulungu ndipo sadzayiwala ntchito zake koma adzasunga malamulo ake.
[8] Iwo asadzakhale monga makolo awo, mʼbado wosamvera ndi wowukira, umene mitima yake inali yosamvera Mulungu, umene mizimu yake inali yosakhulupirika kwa Iye.
[9] Anthu a ku Efereimu, ngakhale ananyamula mauta, anathawabe pa nthawi ya nkhondo;
[10] iwo sanasunge pangano la Mulungu ndipo anakana kukhala mʼmoyo wotsatira lamulo lake.
[11] Anayiwala zimene Iye anachita, zozizwitsa zimene anawaonetsa.
[12] Iyeyo anachita zodabwitsa makolo athu akuona, mʼdziko la Igupto, mʼchigawo cha Zowani.
[13] Anagawa nyanja pakati ndi kudutsitsapo iwowo, Iye anachititsa madzi kuyima chilili ngati khoma.
[14] Anawatsogolera ndi mtambo masana ndi kuwala kwa moto usiku wonse.
[15] Iye anangʼamba miyala mʼchipululu ndi kuwapatsa madzi ochuluka ngati a mʼnyanja zambiri;
[16] Anatulutsa mitsinje kuchokera mʼmingʼalu ya miyala ndi kuyenda madzi ngati mitsinje.
[17] Komabe iwowo anapitiriza kumuchimwira Iye, kuwukira Wammwambamwamba mʼchipululu.
[18] Ananyoza Mulungu mwadala pomuwumiriza kuti awapatse chakudya chimene anachilakalaka.
[19] Iwo anayankhula motsutsana naye ponena kuti, “Kodi Mulungu angatipatse chakudya mʼchipululu?
[20] Iye atamenya thanthwe madzi anatuluka, ndipo mitsinje inadzaza ndi madzi. Koma iye angatipatsenso ife chakudya? Kodi angapereke nyama kwa anthu akewa?”
[21] Yehova atawamva anakwiya kwambiri; moto wake unayaka kutsutsana ndi Yakobo, ndipo mkwiyo wake unauka kutsutsana ndi Israeli,
[22] pakuti iwo sanakhulupirire Mulungu kapena kudalira chipulumutso chake.
[23] Komabe Iye anapereka lamulo kwa mitambo mmwamba ndi kutsekula makomo a mayiko akumwamba;
[24] anagwetsa mana kuti anthu adye, anawapatsa tirigu wakumwamba.
[25] Anthu anadya buledi wa angelo, Iye anawatumizira chakudya chonse chimene akanatha kudya.
[26] Anamasula mphepo ya kummwera kuchokera kumwamba, ndi kutsogolera mphepo ya kummwera mwa mphamvu zake.
[27] Iye anawagwetsera nyama ngati fumbi, mbalame zowuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
[28] Anazibweretsa kwa iwo mʼkati mwa misasa yawo, kuzungulira matenti awo onse.
[29] Iwo anadya mpaka anatsala nazo zochuluka pakuti Iye anawapatsa zimene anazilakalaka.
[30] Koma iwowo anasiya kudya chakudya anachilakalakacho, chakudya chili mʼkamwa mwawobe,
[31] mkwiyo wa Mulungu unawayakira; Iye anapha amphamvu onse pakati pawo, kugwetsa anyamata abwino kwambiri mu Israeli.
[32] Ngakhale zinali chomwechi, iwo anapitirira kuchimwa; ngakhale anaona zozizwitsa zakezo iwowo sanakhulupirirebe.
[33] Kotero Mulungu anachepetsa masiku awo kuti azimirire ngati mpweya. Iye anachepetsa zaka zawo kuti zithere mʼmasautso.
[34] Mulungu atawapha, iwo amamufunafuna Iyeyo; iwo ankatembenukiranso kwa Iye mwachangu.
[35] Ankakumbukira kuti Mulungu ndiye Thanthwe lawo, kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye Mpulumutsi wawo.
[36] Komabe ankamuthyasika ndi pakamwa pawo, kumunamiza ndi malilime awo;
[37] Mitima yawo sinali yokhazikika pa Iye, iwo sanakhulupirike ku pangano lake.
[38] Komabe Iye anali wachifundo; anakhululukira mphulupulu zawo ndipo sanawawononge. Nthawi ndi nthawi Iye anabweza mkwiyo wake ndipo sanawutse ukali wake wonse.
[39] Iye anakumbukira kuti iwo anali anthu chabe, mphepo yopita imene sibwereranso.
[40] Nthawi zambiri iwo ankamuwukira Iye mʼchipululu ndi kumumvetsa chisoni mʼdziko lopanda kanthu!
[41] Kawirikawiri iwo ankamuyesa Mulungu; ankamuputa Woyera wa Israeli.
[42] Sanakumbukire mphamvu zake, tsiku limene Iye anawawombola kwa ozunza,
[43] tsiku limene Iyeyo anaonetsa poyera zizindikiro zozizwitsa zake mu Igupto, zozizwitsa zake mʼchigawo cha Zowani.
[44] Iye anasandutsa mitsinje yawo kukhala magazi; Iwo sanathe kumwa madzi ochokera mʼmitsinje yawo.
[45] Iye anawatumizira magulu a ntchentche zimene zinawawononga, ndiponso achule amene anawasakaza.
[46] Iye anapereka mbewu zawo kwa ziwala, zokolola zawo kwa dzombe.
[47] Iye anawononga mphesa zawo ndi matalala ndiponso mitengo yawo yankhuyu ndi chisanu.
[48] Iye anapereka ngʼombe zawo ku matalala, zoweta zawo ku zingʼaningʼani.
[49] Anakhuthula moto wa ukali wake pa iwo, anawapsera mtima nawakwiyira nʼkuwabweretsera masautso. Zimenezi zinali ngati gulu la angelo osakaza.
[50] Analolera kukwiya, sanawapulumutse ku imfa koma anawapereka ku mliri.
[51] Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto, zipatso zoyamba kucha za mphamvu zawo mʼmatenti a Hamu
[52] Koma Iye anatulutsa anthu ake ngati ziweto; anawatsogolera ngati nkhosa kudutsa mʼchipululu.
[53] Anawatsogolera bwinobwino kotero kuti analibe mantha koma nyanja inamiza adani awo.
[54] Kotero anawafikitsa ku malire a dziko lake loyera, ku dziko lamapiri limene dzanja lake lamanja linawatengera.
[55] Iye anathamangitsa mitundu ya anthu patsogolo pawo ndipo anapereka mayiko awo kwa Aisraeli kuti akhale awo; Iye anakhazikitsa mafuko a Israeli mʼnyumba zawo.
[56] Koma iwo anayesa Mulungu ndi kuwukira Wammwambamwamba; sanasunge malamulo ake.
[57] Anakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo awo, anapotoka monga uta wosakhulupirika.
[58] Anakwiyitsa Iyeyo ndi malo awo opembedzera mafano; anawutsa nsanje yake ndi mafano awo.
[59] Pamene Mulungu anamva zimenezi, anakwiya kwambiri; Iye anakana Israeli kwathunthu.
[60] Anasiya nyumba ya ku Silo, tenti imene Iyeyo anayimanga pakati pa anthu.
[61] Anatumiza mphamvu zake ku ukapolo, ulemerero wake mʼmanja mwa adani.
[62] Anapereka anthu ake ku lupanga; anakwiya kwambiri ndi cholowa chake.
[63] Moto unanyeketsa anyamata awo, ndipo anamwali awo analibe nyimbo za ukwati;
[64] ansembe awo anaphedwa ndi lupanga, ndipo amayi awo amasiye sanathe kulira.
[65] Kenaka Ambuye anakhala ngati akudzuka kutulo, ngati munthu wamphamvu wofuwula chifukwa cha vinyo.
[66] Iye anathamangitsa adani ake; anawachititsa manyazi ku nthawi zonse.
[67] Kenaka Iye anakana matenti a Yosefe, sanasankhe fuko la Efereimu;
[68] Koma anasankha fuko la Yuda, phiri la Ziyoni limene analikonda.
[69] Iye anamanga malo ake opatulika ngati zitunda, dziko limene analikhazikitsa kwamuyaya.
[70] Anasankha Davide mtumiki wake ndi kumuchotsa pakati pa makola ankhosa;
[71] kuchokera koyangʼanira nkhosa anamubweretsa kuti akhale mʼbusa wa anthu ake, Yakobo, wa Israeli cholowa chake.
[72] Ndipo Davide anawaweta ndi mtima wolungama; ndi manja aluso anawatsogolera.