[1] Davide anati: Ine ndimakukondani Inu Yehova, mphamvu zanga.
[2] Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga; Mulungu wanga ndi thanthwe langa mʼmene ndimathawiramo. Chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa, ndi linga langa.
[3] Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando, ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.
[4] Zingwe za imfa zinandizinga; mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
[5] Anandimanga ndi zingwe za ku manda; misampha ya imfa inalimbana nane.
[6] Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova; ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize. Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga; kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake.
[7] Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi, ndipo maziko a mapiri anagwedezeka; ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
[8] Mʼmphuno mwake munatuluka utsi; moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake, makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.
[9] Iye anangʼamba thambo natsika pansi; pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda.
[10] Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka; nawuluka ndi mphepo mwaliwiro.
[11] Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake, chophimba chake chomuzungulira chinali mitambo yakuda ya mlengalenga.
[12] Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake munkachokera matalala, makala amoto ndi ziphaliwali zongʼanima.
[13] Yehova anabangula kumwamba ngati bingu, mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse.
[14] Iye anaponya mivi yake nabalalitsa adani ake, ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa.
[15] Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera; maziko a dziko lapansi anakhala poyera, Yehova atabangula mwaukali, pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwanu.
[16] Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira; anandivuwula mʼmadzi ozama.
[17] Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, adani anga, amene anali amphamvu kuposa ine.
[18] Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto, koma Yehova anali thandizo langa.
[19] Iye anandipititsa kumalo otakasuka; anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane.
[20] Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa; molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.
[21] Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova; ndilibe mlandu wochoka pamaso Mulungu wanga.
[22] Malamulo ake onse ali pamaso panga; sindinasiye malangizo ake.
[23] Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.
[24] Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa, molingana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake.
[25] Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu; kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,
[26] kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu, koma kwa achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.
[27] Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa, koma anthu amtima odzikuza mumawatsitsa.
[28] Inu Yehova, sungani nyale yanga kuti iziyakabe; Mulungu wanga wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.
[29] Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo; ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.
[30] Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro; mawu a Yehova alibe cholakwika. Iye ndi chishango kwa onse amene amathawira kwa Iye.
[31] Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova? Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?
[32] Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu ndi kulungamitsa njira yanga.
[33] Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi; Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri.
[34] Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo; manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo.
[35] Inu mumandipatsa chishango chachipambano, ndipo dzanja lanu lamanja limandichirikiza; mumawerama pansi kundikuza.
[36] Munakulitsa njira yoyendamo ine, kuti mapazi anga asaguluke.
[37] Ndinathamangitsa adani anga ndi kuwapitirira; sindinabwerere mpaka atawonongedwa.
[38] Ndinakantha adaniwo kotero kuti sanathenso kudzuka; anagwera pa mapazi anga.
[39] Inu munandiveka ndi mphamvu yokachitira nkhondo, munachititsa kuti ndigonjetse adani anga.
[40] Inu munachititsa adani anga kutembenuka, kuonetsa misana yawo pothawa, ndipo ine ndinawononga adani angawo.
[41] Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa. Analirira kwa Yehova koma sanawayankhe.
[42] Ine ndinawaperesa ngati fumbi lowuluka ndi mphepo. Ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.
[43] Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa anthu; mwandisandutsa kukhala mtsogoleri wa anthu a mitundu ina. Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
[44] Alendo amadzipereka okha pamaso panga; akangomva za ine amandigonjera.
[45] Iwo onse anataya mtima; anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.
[46] Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa! Akuzike Mulungu Mpulumutsi wanga!
[47] Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango, amene amagonjetsa anthu a mitundu yonse amene ali pansi pa ulamuliro wanga,
[48] amene amandipulumutsa mʼmanja mwa adani anga. Inu munandikuza kuposa adani anga; munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
[49] Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa anthu a mitundu ina, Inu Yehova; ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
[50] Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake; amaonetsa chikondi chosasinthika kwa wodzozedwa wake, kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.