Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:22

[1] Imbani mwachimwemwe kwa Mulungu mphamvu yathu; Fuwulani mokweza kwa Mulungu wa Yakobo!

[2] Yambani nyimbo, imbani tambolini imbani pangwe wolira bwino ndi zeze.

[3] Imbani lipenga la nyanga ya nkhosa yayimuna pa mwezi watsopano, ndi pamene mwezi waoneka wonse, pa tsiku la phwando;

[4] ili ndi lamulo kwa Israeli, langizo la Mulungu wa Yakobo.

[5] Iye anapereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe pamene anatuluka kulimbana ndi Igupto, kumene tinamva chiyankhulo chimene sitinachidziwe.

[6] Iye akunena kuti, “Ine ndinachotsa zolemetsa pa mapewa awo; Manja awo anamasulidwa mʼdengu.

[7] Pa mavuto anu munayitana ndipo ndinakulanditsani, ndinakuyankhani kuchokera mʼmitambo ya mabingu; ndinakuyesani pa madzi a ku Meriba. q4 Sela

[8] “Imvani anthu anga, ndipo ndidzakuchenjezani ngati mungathe kumvetsera, Inu Israeli!

[9] Musadzakhale ndi mulungu wachilendo pakati panu; musadzagwadire mulungu wina.

[10] Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto. Yasamani kukamwa kwanu ndipo ndidzakudyetsani.

[11] “Koma anthu anga sanandimvere; Israeli sanandigonjere.

[12] Kotero ndinawasiya ndi mitima yawo yosamverayo kuti atsate zimene ankafuna.

[13] “Anthu anga akanangondimvera, Israeli akanatsatira njira zanga,

[14] nʼkanafulumira motani kuti ndigonjetse adani awo ndi kutembenuza mkono wanga kulimbana ndi amaliwongo!

[15] Iwo amene amadana ndi Yehova akanakhwinyata pamaso pake, ndipo chilango chawo chinakakhala mpaka kalekale.

[16] Koma inu mukanadyetsedwa tirigu wabwino kwambiri; ndikanakukhutitsani ndi uchi wochokera pa thanthwe.”

Masalimo — Chapters