Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:08

[1] Tamandani Yehova. Mutamandeni, inu atumiki a Yehova, tamandani dzina la Yehova.

[2] Yehova atamandidwe, kuyambira tsopano mpaka muyaya.

[3] Kuyambira ku matulukiro a dzuwa mpaka ku malowero ake, dzina la Yehova liyenera kutamandidwa.

[4] Yehova wakwezeka pa anthu a mitundu yonse, ulemerero wake ndi woposa mayiko akumwamba.

[5] Ndani wofanana ndi Yehova Mulungu wathu, Iye amene amakhala mwaufumu mmwamba?

[6] amene amawerama pansi kuyangʼana miyamba ndi dziko lapansi?

[7] Iye amakweza munthu wosauka kuchoka pa fumbi ndi kutukula munthu wosowa kuchoka pa dzala;

[8] amawakhazika pamodzi ndi mafumu, pamodzi ndi mafumu a anthu ake.

[9] Amakhazikitsa mayi wosabereka mʼnyumba yake monga mayi wa ana wosangalala. Tamandani Yehova.

Masalimo — Chapters