Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:13

[1] Inu Yehova, achulukadi adani anga! Achulukadi amene andiwukira!

[2] Ambiri akunena za ine kuti, “Mulungu sadzamupulumutsa.” q4 Sela

[3] Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza, Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula.

[4] Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera. q4 Sela

[5] Ine ndimagona ndi kupeza tulo; ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza.

[6] Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse.

[7] Dzukani, Inu Yehova! Pulumutseni, Inu Mulungu wanga. Akantheni adani anga onse pa msagwada; gululani mano a anthu oyipa.

[8] Chipulumutso chimachokera kwa Yehova. Madalitso akhale pa anthu anu. q4 Sela

Masalimo — Chapters