Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:24

[1] Mulungu amene ndimakutamandani, musakhale chete,

[2] pakuti anthu oyipa ndi achinyengo atsekula pakamwa pawo kutsutsana nane; iwo ayankhula motsutsana nane ndi malilime abodza.

[3] Andizungulira ndi mawu audani, amandinena popanda chifukwa.

[4] Mʼmalo mwa chikondi changa amandineneza, koma ine ndine munthu wapemphero.

[5] Iwo amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino, ndi udani mʼmalo mwa chikondi changa.

[6] Sankhani munthu woyipa kuti amutsutse iye; lolani wotsutsa ayime ku dzanja lake lamanja.

[7] Pamene aweruzidwa, apezeke kuti ndi wolakwa, ndipo mapemphero ake amutsutse.

[8] Masiku ake akhale owerengeka; munthu wina atenge malo ake a utsogoleri.

[9] Ana ake akhale amasiye ndipo mkazi wake akhale wopanda mwamuna.

[10] Ana ake akhale oyendayenda ndi opemphapempha; apirikitsidwe kuchoka pa mabwinja a nyumba zawo.

[11] Wokongoza alande zonse zimene ali nazo; alendo afunkhe ntchito za manja ake.

[12] Pasapezeke ndi mmodzi yemwe womukomera mtima kapena kumvera chisoni ana ake amasiye.

[13] Zidzukulu zake zithe nʼkufa, mayina awo afafanizidwe mu mʼbado wotsatirawo.

[14] Mphulupulu za makolo ake zikumbukiridwe pamaso pa Yehova; tchimo la amayi ake lisadzafafanizidwe.

[15] Machimo awo akhale pamaso pa Yehova nthawi zonse, kuti Iye achotse chikumbutso chawo pa dziko lapansi.

[16] Pakuti iye sanaganizirepo zochita chifundo, koma anazunza mpaka kuwapha anthu osauka ndi osweka mtima.

[17] Anakonda kutemberera, matembererowo abwerere kwa iye; sanakondwe nʼkudalitsa anthu ena, choncho madalitso akhale kutali naye.

[18] Anavala kutemberera ngati chovala; kutemberera kunalowa mʼthupi lake ngati madzi, kulowa mʼmafupa ake ngati mafuta.

[19] Matemberero akhale ngati chofunda chodzikutira nacho, ngati lamba wovala tsiku ndi tsiku.

[20] Awa akhale malipiro ochokera kwa Yehova pa onditsutsa anga, kwa iwo amene amayankhula zoyipa za ine.

[21] Koma Inu Ambuye Wamphamvuzonse, muchite nane molingana ndi dzina lanu, chifukwa cha ubwino wa chikondi chanu, pulumutseni.

[22] Pakuti ndine wosauka ndi wosowa, ndipo mtima wanga ukuwawa mʼkati mwanga.

[23] Ndikuzimirira ngati mthunzi wa kumadzulo, ndapirikitsidwa ngati dzombe.

[24] Mawondo anga afowoka chifukwa cha kusala zakudya, thupi langa lawonda ndi mutu wanga womwe.

[25] Ndine chinthu chotonzedwa kwa otsutsana nane; akandiona, amapukusa mitu yawo.

[26] Thandizeni Inu Yehova Mulungu wanga; pulumutseni molingana ndi chikondi chanu.

[27] Adaniwo adziwe kuti limeneli ndi dzanja lanu, kuti Inu Yehova mwachita zimenezi.

[28] Angathe kutemberera, koma Inu mudzadalitsa; pamene iwo andiputa adzachititsidwa manyazi, koma mtumiki wanu adzasangalala.

[29] Onditsutsa adzavekedwa mnyozo, ndipo adzadzifunditsa manyazi ngati chovala.

[30] Ndi pakamwa panga ndidzathokoza Yehova kwambiri; ndidzamutamanda mʼgulu lalikulu la anthu.

[31] Popeza Iye amayima ku dzanja lamanja la munthu wosowayo, kupulumutsa moyo wake kwa iwo amene agamula molakwa.

Masalimo — Chapters