Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:27

[1] Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.

[2] Israeli anene kuti: “Chikondi chake ndi chosatha.”

[3] Banja la Aaroni linene kuti, “Chikondi chake ndi chosatha.”

[4] Iwo amene amaopa Yehova anene kuti: “Chikondi chake ndi chosatha.”

[5] Ndili mʼmasautso anga ndinalirira Yehova, ndipo Iye anayankha pondichotsa mʼmasautsowo.

[6] Yehova ali nane; sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?

[7] Yehova ali nane; Iye ndiye thandizo langa. Ndidzayangʼana adani anga mwachipambano.

[8] Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova kusiyana ndi kudalira munthu.

[9] Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova kusiyana ndi kudalira mafumu.

[10] Anthu a mitundu yonse anandizinga, koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga.

[11] Anandizinga mbali zonse, koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga.

[12] Anandizinga ngati njuchi, koma anatha msanga ngati moto wapaminga; mʼdzina la Yehova ndinawawononga.

[13] Anandikankha uku ndi uko ndipo ndinali pafupi kugwa, koma Yehova anandithandiza.

[14] Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; Iye wakhala chipulumutso changa.

[15] Mfuwu wachimwemwe ndi chipambano ukumveka mʼmatenti a anthu olungama mtima kuti: “Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!

[16] Dzanja lamanja la Yehova latukulidwa mmwamba Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!”

[17] Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo ndipo ndidzalalika za ntchito ya Yehova.

[18] Yehova wandilanga koopsa, koma sanandipereke ku imfa.

[19] Tsekulireni zipata zachilungamo, kuti ndifike kudzayamika Yehova.

[20] Ichi ndicho chipata cha Yehova chimene olungama mtima okha adzalowerapo.

[21] Ndidzakuyamikani chifukwa Inu munandiyankha; mwakhala chipulumutso changa.

[22] Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana wasanduka wapangodya;

[23] Yehova ndiye wachita zimenezi ndipo nʼzodabwitsa pamaso pathu.

[24] Lero ndiye tsiku limene Yehova walipanga; tiyeni tikondwere ndi kusangalala nalo.

[25] Inu Yehova, tipulumutseni; Yehova, tipambanitseni.

[26] Wodala amene akubwera mʼdzina la Yehova. Tikukudalitsani kuchokera ku nyumba ya Yehova.

[27] Yehova ndi Mulungu, ndipo kuwala kwake kwatiwunikira Ife. Lowani nawo pa mʼdipiti wa ku chikondwerero mutanyamula nthambi mʼdzanja lanu, mpaka ku nyanga za guwa.

[28] Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani; Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakukwezani.

[29] Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.

Masalimo — Chapters