Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:22

[1] Inu Yehova, ndinu Mulungu wobwezera chilango, Inu Mulungu amene mumabwezera chilango, wonetsani kuwala kwanu.

[2] Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi; bwezerani kwa odzikuza zowayenera.

[3] Kodi mpaka liti anthu oyipa Inu Yehova, mpaka liti anthu oyipa adzalumpha ndi chimwemwe?

[4] Amakhuthula mawu onyada; onse ochita zoyipa ndi odzaza ndi kudzikuza.

[5] Amaphwanya anthu anu, Inu Yehova; amapondereza cholowa chanu.

[6] Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko; amapha ana amasiye.

[7] Iwo amati, “Yehova sakuona; Mulungu wa Yakobo salabadirako.”

[8] Samalani, inu anthu opanda nzeru pakati pa anthu; zitsiru inu, kodi mudzakhala liti anzeru?

[9] Kodi Iye amene anapanga khutu sangathe kumva? Kodi Iye amene anapanga diso sangathe kuona?

[10] Kodi Iye amene amalangiza mitundu ya anthu sangathenso kulanga? Kodi Iye amene amaphunzitsa munthu angasowe nzeru?

[11] Yehova amadziwa maganizo a munthu; Iye amadziwa kuti maganizowo ndi achabechabe.

[12] Wodala munthu amene Inu Yehova mumamulangiza, munthu amene mumamuphunzitsa kuchokera mulamulo lanu;

[13] mumamupumitsa pa nthawi ya mavuto, mpaka woyipa atakumbiridwa dzenje.

[14] Pakuti Yehova sadzawakana anthu ake; Iye sadzasiya cholowa chake.

[15] Chiweruzo chidzakhazikikanso pa chilungamo, ndipo onse olungama mtima adzachitsata.

[16] Ndani adzadzuka chifukwa cha ine kulimbana ndi anthu oyipa? Ndani adzayimirira mʼmalo mwanga kulimbana ndi anthu ochita zoyipa?

[17] Yehova akanapanda kundithandiza, bwenzi nditakakhala msanga ku malo achete a imfa.

[18] Ndikanena kuti, “Phazi langa likuterereka,” chikondi chanu, Inu Yehova, chimandichirikiza.

[19] Pamene nkhawa inakula mʼkati mwanga, chitonthozo chanu chinabweretsa chimwemwe mʼmoyo mwanga.

[20] Kodi mpando waufumu woyipa ungathe kugwirizana nanu umene umabweretsa masautso chifukwa cha malamulo ake?

[21] Iwo amasonkhana pamodzi kulimbana ndi wolungama ndi kugamula kuti wosalakwa aphedwe.

[22] Koma Yehova wakhala linga langa, ndipo Mulungu ndiye thanthwe limene ndimathawirako.

[23] Iye adzawabwezera chifukwa cha machimo awo ndi kuwawononga chifukwa cha kuyipa kwawo; Yehova Mulungu wathu adzawawononga.

Masalimo — Chapters