Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:46

[1] Weruzeni Inu Yehova pakuti ndakhala moyo wosalakwa. Ndadalira Yehova popanda kugwedezeka.

[2] Patseni mayeso, Inu Yehova ndipo ndiyeseni, santhulani mtima wanga ndi maganizo anga;

[3] pakuti chikondi chanu chili pamaso panga nthawi zonse, ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu nthawi zonse.

[4] Ine sindikhala pansi pamodzi ndi anthu achinyengo, kapena kufunsa nzeru kwa achiphamaso.

[5] Ndimanyansidwa ndi msonkhano wa anthu ochita zoyipa ndipo ndimakana kukhala pansi pamodzi ndi oyipa.

[6] Ndimasamba mʼmanja mwanga kuonetsa kusalakwa kwanga ndi kupita kukatumikira pa guwa lanu la nsembe, Inu Yehova,

[7] kulengeza mofuwula za matamando anu ndi kuwuza onse za ntchito zanu zodabwitsa.

[8] Ndimakonda Nyumba imene Inu Yehova mumakhalamo, malo amene ulemerero wanu umapezekako.

[9] Musachotse moyo wanga pamodzi ndi ochimwa, moyo wanga pamodzi ndi anthu akupha anzawo,

[10] amene mʼmanja mwawo muli ndondomeko zoyipa, dzanja lawo lamanja ladzaza ndi ziphuphu.

[11] Koma ine ndimakhala moyo wosalakwa; mu msonkhano wa anthu anu ndidzatamanda Yehova.

[12] Ndayima pa malo wopanda zovuta ndipo ndidzatamanda Yehova mu msonkhano waukulu.

Masalimo — Chapters