[1] Ndidzayimba za chikondi chachikulu cha Yehova kwamuyaya; ndi pakamwa panga ndidzachititsa kuti kukhulupirika kwanu kudziwike ku mibado yonse.
[2] Ndidzalalikira kuti chikondi chanu chidzakhazikika mpaka muyaya, kuti Inu munakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba kwenikweniko.
[3] Inu munati, “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga, ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti,
[4] ‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya. Ndidzachititsa kuti mpando wako waufumu ukhazikike ku mibado yonse,’ ” q4 Sela.
[5] Mayiko akumwamba amatamanda zozizwitsa zanu Yehova, kukhulupirika kwanunso, mu msonkhano wa oyera mtima anu.
[6] Pakuti ndani mu mlengalenga angalingane ndi Yehova? Ndani wofanana ndi Yehova pakati pa zolengedwa zakumwamba?
[7] Mu msonkhano wa oyera mtima Mulungu amaopedwa kwambiri; Iye ndiye wochititsa mantha kupambana onse amene amuzungulira.
[8] Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, ndani wofanana nanu? Yehova ndinu wamphamvu ndipo kukhulupirika kwanu kwakuzungulirani.
[9] Mumalamula nyanja ya mafunde awukali; pamene mafunde ake awundana Inu mumawakhalitsa bata.
[10] Munaphwanya Rahabe monga munthu wophedwa; ndi dzanja lanu lamphamvu munabalalitsa adani anu.
[11] Mayiko akumwamba ndi anu ndiponso dziko lapansi ndi lanu; munapanga dziko lonse ndi zonse zili mʼmenemo.
[12] Munalenga Kumpoto ndi Kummwera; Tabori ndi Herimoni akuyimba ndi chimwemwe pa dzina lanu.
[13] Mkono wanu ndi wamphamvu; dzanja lanu ndi lamphamvu, dzanja lanu lamanja ndi lopambana.
[14] Chilungamo ndi chiweruzo cholungama ndiye maziko a mpando wanu waufumu; chikondi ndi kukhulupirika zimayenda patsogolo panu.
[15] Ndi odala amene aphunzira kuyamika Inu, amene amayenda mʼkuwunika kwa nkhope yanu Yehova.
[16] Amakondwera mʼdzina lanu tsiku lonse lathunthu; amasangalala koposa mʼchilungamo chanu.
[17] Pakuti Inu ndiye ulemerero wawo ndi mphamvu yawo ndipo mwa kukoma mtima kwanu Inu mumakweza nyanga yathu.
[18] Ndithudi, chishango chathu ndi cha Yehova, Mfumu yathu kwa Woyerayo wa Israeli.
[19] Kale munayankhula mʼmasomphenya, kwa anthu anu okhulupirika munati, “Ndapatsa mphamvu wankhondo; ndakweza mnyamata wochokera pakati pa anthu.
[20] Ndamupeza mtumiki wanga Davide; ndamudzoza ndi mafuta opatulika.
[21] Dzanja langa lidzamuchirikiza; zoonadi, mkono wanga udzamupatsa mphamvu.
[22] Adani sadzamulamula kuti apereke msonkho; anthu oyipa sadzamusautsa.
[23] Ndidzaphwanya adani ake pamaso pake ndi kukantha otsutsana naye.
[24] Chikondi changa chokhulupirika chidzakhala naye, ndipo kudzera mʼdzina langa nyanga yake idzakwezedwa.
[25] Ndidzayika dzanja lake pa nyanja, dzanja lake lamanja pa mitsinje.
[26] Iyeyo adzafuwula kwa Ine kuti, ‘Ndinu Atate anga, Mulungu wanga, Thanthwe ndi Chipulumutso changa.’
[27] Ndidzamuyika kuti akhale mwana wanga woyamba kubadwa; wokwezedwa kwambiri pakati pa mafumu a dziko lapansi.
[28] Ndidzamusungira chifundo changa kwamuyaya, ndipo pangano langa ndi iye silidzatha.
[29] Ine ndidzakhazikitsa zidzukulu zake mpaka muyaya, mpando wake waufumu ngati masiku a miyamba.
[30] “Ngati ana ake adzataya lamulo langa ndi kusatsatira malangizo anga,
[31] ngati adzaswa malamulo anga ndi kulephera kusunga ziphunzitso zanga,
[32] Ine ndidzalanga tchimo lawo ndi ndodo, mphulupulu zawo powakwapula.
[33] Koma sindidzachotsa chikondi changa pa iye, kapena kukhala wosakhulupirika kwa iyeyo.
[34] Sindidzaswa pangano langa kapena kusintha zimene milomo yanga yayankhula.
[35] Ndinalumbira kamodzi mwa kuyera kwanga ndipo sindidzanama kwa Davide,
[36] kuti zidzukulu zake zidzakhale kwamuyaya ndipo mpando wake waufumu udzakhazikika pamaso panga ngati dzuwa;
[37] udzakhazikika kwamuyaya monga mwezi, mboni yokhulupirika mʼmitambo. q4 Sela
[38] “Koma tsopano Inu mwamukana, mwamutaya, mwamukwiyira kwambiri wodzozedwa wanu.
[39] Mwakana pangano ndi mtumiki wanu ndipo mwadetsa mʼfumbi chipewa chake chaufumu.
[40] Inu mwagumula makoma ake onse ndipo mwasandutsa bwinja malinga ake.
[41] Onse amene amadutsa amalanda zinthu zake; iye wakhala chotonzedwa cha anansi ake.
[42] Mwakweza dzanja lamanja la adani ake; mwachititsa kuti adani ake akondwere.
[43] Mwabunthitsa lupanga lake, simunamuthandize pa nkhondo.
[44] Inu mwathetsa kukongola kwa ulemerero wake ndipo mwagwetsa pansi mpando wake waufumu.
[45] Mwachepetsa masiku a unyamata wake; mwamuphimba ndi chofunda chochititsa manyazi. q4 Sela
[46] “Mpaka liti Yehova? Kodi mudzadzibisa mpaka kalekale? Mpaka liti ukali wanu udzayaka ngati moto?
[47] Kumbukirani kuti masiku a moyo wanga ndi ochepa pakuti munalenga kwachabe anthu onse!
[48] Kodi ndi munthu uti angakhale ndi moyo ndi kusaona imfa? Kapena kudzipulumutsa yekha ku mphamvu ya manda? q4 Sela
[49] Inu Ambuye kodi chili kuti chikondi chanu chachikulu choyamba chija, chimene mwa kukhulupirika kwanu munalumbira kwa Davide?
[50] Kumbukirani, Ambuye momwe mtumiki wanu wanyozedwera, momwe ndakhalira ndi kusunga mu mtima mwanga mawu a pangano a anthu a mitundu yonse,
[51] mawu achipongwe amene adani anu akhala akunyoza, Inu Yehova, ndi mawu amene akhala akunyoza mayendedwe onse a wodzozedwa wanu.
[52] “Matamando akhale kwa Yehova mpaka muyaya!” Ameni ndi Ameni.