Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:32

[1] Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa; dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zamuchitira chipulumutso.

[2] Yehova waonetsa chipulumutso chake ndipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina.

[3] Iye wakumbukira chikondi chake ndi kukhulupirika kwake pa Aisraeli; malekezero onse a dziko lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

[4] Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi, muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera.

[5] Imbirani Yehova nyimbo ndi zeze, ndi zeze ndi mawu a kuyimba,

[6] ndi malipenga ndi kuliza kwa nyanga ya nkhosa yayimuna fuwulani mwachimwemwe pamaso pa Yehova Mfumu.

[7] Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo, dziko lonse ndi onse amene amakhala mʼmenemo.

[8] Mitsinje iwombe mʼmanja mwawo, mapiri ayimbe pamodzi mwachimwemwe;

[9] izo ziyimbe pamaso pa Yehova, pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo, ndi mitundu ya anthu mosakondera.

Masalimo — Chapters