[1] Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu yanga; ndidzatamanda dzina lanu ku nthawi za nthawi.
[2] Ndidzakutamandani tsiku ndi tsiku ndi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.
[3] Yehova ndi wamkulu ndi woyenera matamando onse; ukulu wake palibe angawumvetsetse.
[4] Mʼbado wina udzayamikira ntchito yanu kwa mʼbado wina; Iwo adzafotokoza za machitidwe anu amphamvu.
[5] Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu, ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.
[6] Iwo adzafotokoza za mphamvu ya ntchito zanu zoopsa kwambiri, ndipo ine ndidzalengeza za ntchito zanu zazikulu.
[7] Adzakondwerera kuchuluka kwa ubwino wanu, ndi kuyimba mwachimwemwe za chilungamo chanu.
[8] Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika.
[9] Yehova ndi wabwino kwa onse; amachitira chifundo zonse zimene anazipanga.
[10] Zonse zimene munazipanga zidzakutamandani, Inu Yehova; oyera mtima adzakulemekezani.
[11] Iwo adzafotokoza za ulemerero wa ufumu wanu ndi kuyankhula za mphamvu yanu,
[12] kuti anthu onse adziwe za machitidwe anu amphamvu ndi ulemerero wokongola wa ufumu wanu.
[13] Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya, ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse. Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onse ndi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.
[14] Yehova amagwiriziza onse amene akugwa ndipo amakweza onse otsitsidwa.
[15] Maso a onse amayangʼana kwa Inu, ndipo Inu mumawapatsa chakudya chawo pa nthawi yoyenera.
[16] Mumatsekula dzanja lanu ndi kukwaniritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.
[17] Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse, ndi wokonda zonse zimene anazipanga.
[18] Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana, onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi.
[19] Iye amakwaniritsa zokhumba za iwo amene amamuopa; amamva kulira kwawo ndi kuwapulumutsa.
[20] Yehova amayangʼana onse amene amamukonda koma adzawononga anthu onse oyipa.
[21] Pakamwa panga padzayankhula zotamanda Yehova. Cholengedwa chilichonse chitamande dzina lake loyera ku nthawi za nthawi.