Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 0:49

[1] Odala ndi onse amene amaopa Yehova, amene amayenda mʼnjira zake.

[2] Udzadya chipatso cha ntchito yako; madalitso ndi chuma zidzakhala zako.

[3] Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka mʼkati mwa nyumba yako; ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi kuzungulira tebulo lako.

[4] Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa amene amaopa Yehova.

[5] Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni masiku onse a moyo wako; uwone zokoma za Yerusalemu,

[6] ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako. Mtendere ukhale ndi Israeli.

Masalimo — Chapters