Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 0:55

[1] Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni, tinali ngati amene akulota.

[2] Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka; malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe. Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti, “Yehova wawachitira zinthu zazikulu.”

[3] Yehova watichitira zinthu zazikulu, ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe.

[4] Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova, monga mitsinje ya ku Negevi.

[5] Iwo amene amafesa akulira, adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.

[6] Iye amene amayendayenda nalira, atanyamula mbewu yokafesa, adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe, atanyamula mitolo yake.

Masalimo — Chapters