Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:41

[1] Ambuye, mwakhala muli malo athu okhalamo pa mibado yonse.

[2] Mapiri asanabadwe, musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse, kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.

[3] Inu mumabwezera anthu ku fumbi, mumati, “Bwerera ku fumbi iwe mwana wa munthu.”

[4] Pakuti zaka 1,000 pamaso panu zili ngati tsiku limene lapita kapena ngati kamphindi ka usiku.

[5] Inu mumasesa anthu mʼtulo ta imfa, iwo ali ngati udzu watsopano wa mmawa,

[6] ngakhale kuti mmawa umaphuka watsopano, pofika madzulo wauma ndi kufota.

[7] Ife tathedwa ndi mkwiyo wanu; ndipo taopsezedwa ndi kuyipidwa kwanu.

[8] Mwayika mphulupulu zathu pamaso panu, machimo athu obisika poonekera pamaso panu.

[9] Masiku athu onse amatha ali pansi pa ukali wanu; timatsiriza zaka zathu ndi kubuwula.

[10] Kuchuluka kwa masiku athu ndi 70, kapena 80 ngati tili ndi mphamvu; komabe zaka zonsezi ndi za mavuto ndi nkhawa, zimatha mofulumira ndipo ife timawulukira kutali.

[11] Kodi ndani amadziwa mphamvu ya mkwiyo wanu? Pakuti ukali wanu ndi waukulu ngati ulemu umene uyenera Inu.

[12] Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola, kuti tikhale ndi mtima wanzeru.

[13] Lezani mtima Inu Yehova! Kodi mudzatikwiyira mpaka liti? Achitireni chifundo atumiki anu.

[14] Mutikhutitse mmawa ndi chikondi chanu chosatha, kuti tiyimbe ndi chimwemwe ndi kukhala okondwa masiku athu onse.

[15] Tisangalatseni masiku ambiri monga masiku amene mwatisautsa, kwa zaka zambiri monga momwe tinaonera mavuto.

[16] Ntchito zanu zionetsedwe kwa atumiki anu, kukongola kwanu kwa ana awo.

[17] Kukoma mtima kwa Ambuye Mulungu wathu kukhale pa ife; tikhazikitsireni ntchito ya manja athu; inde, khazikitsani ntchito ya manja athu.

Masalimo — Chapters