Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:40

[1] Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, moona mtima ine ndimakufunafunani; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka inu, mʼdziko lowuma ndi lotopetsa kumene kulibe madzi.

[2] Inu ndinakuonani ku malo anu opatulika ndipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.

[3] Chifukwa chikondi chanu ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.

[4] Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga, ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga.

[5] Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona. Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya.

[6] Pa bedi panga ndimakumbukira inu; ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku.

[7] Chifukwa ndinu thandizo langa, ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu.

[8] Moyo wanga umakangamira Inu; dzanja lanu lamanja limandigwiriziza.

[9] Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa; adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi.

[10] Iwo adzaperekedwa ku lupanga ndi kukhala chakudya cha ankhandwe.

[11] Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu; onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo, koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa.

Masalimo — Chapters