[1] Imbirani Yehova mokondwera Inu olungama, nʼkoyenera kuti owongoka mtima azitamanda Iyeyo.
[2] Mutamandeni Yehova ndi pangwe; muyimbireni Iye nyimbo pa zeze wa zingwe khumi.
[3] Muyimbireni nyimbo yatsopano; imbani mwaluso, ndipo fuwulani mwachimwemwe.
[4] Pakuti mawu a Yehova ndi olungama ndi owona; Iye ndi wokhulupirika pa zonse zimene amachita.
[5] Yehova amakonda chilungamo ndipo amaweruza molungama; dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chake chosatha.
[6] Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa, zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.
[7] Iye amasonkhanitsa pamodzi madzi a mʼnyanja mʼmitsuko; amayika zozama mʼnyumba zosungiramo.
[8] Dziko lonse lapansi liope Yehova; anthu onse amulemekeze Iye.
[9] Pakuti Iye anayankhula ndipo zinakhalapo; Iye analamulira ndipo zinakhazikika.
[10] Yehova amalepheretsa chikonzero cha anthu a mitundu ina; Iye amaphwanya zolinga za anthu ambiri.
[11] Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya, zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse.
[12] Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova, anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake.
[13] Kuchokera kumwamba Yehova amayangʼana pansi ndi kuona anthu onse;
[14] kuchokera ku malo ake okhalako Iye amayangʼanira onse amene amakhala pa dziko lapansi.
[15] Iye amene amapanga mitima ya onse, amaona zonse zimene akuchita.
[16] Palibe mfumu imene imapulumutsidwa chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo; palibe msilikali amene amathawa ndi mphamvu zake zazikulu.
[17] Kavalo ndi chiyembekezo cha chabechabe cha chipulumutso, ngakhale ali ndi mphamvu yayikulu sangathe kupulumutsa.
[18] Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye; amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha,
[19] kuwawombola iwo ku imfa ndi kuwasunga ndi moyo nthawi ya njala.
[20] Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo; Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu.
[21] Mwa Iye mitima yathu imakondwera, pakuti ife timadalira dzina lake loyera.
[22] Chikondi chanu chosatha chikhale pa ife Inu Yehova, pamene tikuyembekeza kwa Inu.