Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:47

[1] Yehova munakomera mtima dziko lanu; munabwezeretsa ulemerero wa Yakobo.

[2] Munakhululukira mphulupulu za anthu anu ndi kuphimba machimo awo onse. q4 Sela

[3] Munayika pambali ukali wanu wonse ndi kutembenuka kuchoka ku mkwiyo wanu woopsa.

[4] Tibwezeretseninso mwakale Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, ndipo mutichotsere mkwiyo wanu.

[5] Kodi mudzatikwiyira mpaka liti? Kodi mudzapitiriza kukwiya pa mibado yathu yonse?

[6] Kodi simudzatitsitsimutsanso, kuti anthu anu asangalale mwa Inu?

[7] Tionetseni chikondi chanu chosatha, Inu Yehova, ndipo tipatseni chipulumutso chanu.

[8] Ndidzamvetsera zimene Yehova Mulungu adzanena; Iye amalonjeza mtendere kwa anthu ake, oyera mtima ake, koma musawalole kuti abwerere ku zopusa.

[9] Ndithu chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo amene amaopa Iye, kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu.

[10] Chikondi ndi kukhulupirika zimakumana pamodzi; chilungamo ndi mtendere zimapsompsonana.

[11] Kukhulupirika kumatumphuka kuchokera ku dziko lapansi, ndipo chilungamo chimayangʼana pansi kuchokera kumwamba.

[12] Ndithu Yehova adzapereka chimene chili chabwino, ndipo dziko lathu lidzapereka zokolola zake.

[13] Wolungama amapita patsogolo pake ndi kukonza njira za mapazi ake.

Masalimo — Chapters