[1] Kwa ife ayi Yehova, kwa ife ayi koma ulemerero ukhale pa dzina lanu, chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika ndiponso chifukwa cha kukhulupirika kwanu.
[2] Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akunena kuti, “Mulungu wawo ali kuti?”
[3] Mulungu wathu ali kumwamba; Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.
[4] Koma mafano awo ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu.
[5] Pakamwa ali napo koma sayankhula, maso ali nawo koma sapenya;
[6] makutu ali nawo koma samva, mphuno ali nazo koma sanunkhiza;
[7] manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu; mapazi ali nawo koma sayenda; kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu.
[8] Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo, chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.
[9] Inu Aisraeli, dalirani Yehova; Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
[10] Iwe nyumba ya Aaroni, dalira Yehova; Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.
[11] Inu amene mumaopa Iye, dalirani Yehova; Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
[12] Yehova watikumbukira ndipo adzatidalitsa: adzadalitsa nyumba ya Israeli, adzadalitsa nyumba ya Aaroni,
[13] adzadalitsa iwo amene amaopa Yehova; aangʼono ndi aakulu omwe.
[14] Yehova akuwonjezereni madalitso; inuyo pamodzi ndi ana anu.
[15] Mudalitsidwe ndi Yehova, Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
[16] Kumwamba ndi kwa Yehova, koma dziko lapansi Iye walipereka kwa anthu.
[17] Si anthu akufa amene amatamanda Yehova, amene amatsikira kuli chete;
[18] ndi ife amene timatamanda Yehova, kuyambira tsopano mpaka muyaya. Tamandani Yehova.