Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:29

[1] Ndinati, “Ndidzasamalira njira zanga ndipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe; ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekerero nthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga.”

[2] Koma pamene ndinali chete osanena ngakhale kanthu kalikonse kabwino mavuto anga anachulukirabe.

[3] Mtima wanga unatentha mʼkati mwanga, ndipo pamene ndinkalingalira, moto unayaka; kenaka ndinayankhula ndi lilime langa:

[4] “Yehova ndionetseni mathero a moyo wanga ndi chiwerengero cha masiku anga; mundidziwitse kuti moyo wanga ndi wosakhalitsa motani.

[5] Inu mwachititsa kuti masiku anga akhale ochepa kwambiri, kutalika kwa zaka zanga ndi kopanda phindu pamaso panu; moyo wa munthu aliyense ndi waufupi. q4 Sela

[6] Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku: Iye amangovutika koma popanda phindu; amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani.

[7] “Koma tsopano Ambuye kodi ndifunanso chiyani? Chiyembekezo changa chili mwa Inu.

[8] Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse; musandisandutse chonyozeka kwa opusa.

[9] Ine ndinali chete; sindinatsekule pakamwa panga pakuti Inu ndinu amene mwachita zimenezi.

[10] Chotsani mkwapulo wanu pa ine; ndagonjetsedwa ndi nkhonya ya dzanja lanu.

[11] Inu mumadzudzula ndi kulanga anthu chifukwa cha tchimo lawo; mumawononga chuma chawo monga njenjete; munthu aliyense ali ngati mpweya. q4 Sela

[12] “Imvani pemphero langa Inu Yehova, mverani kulira kwanga kopempha thandizo; musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu, popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa; monga anachitira makolo anga onse.

[13] Musandiyangʼane mwaukali, choncho ndidzatha kusangalala ndisanafe ndi kuyiwalika.”

Masalimo — Chapters