Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 0:50

[1] Ndimafuwulira kwa Yehova mʼmasautso anga, ndipo Iye amandiyankha.

[2] Pulumutseni Yehova ku milomo yabodza, ndi kwa anthu achinyengo.

[3] Kodi adzakuchitani chiyani, ndipo adzawonjezerapo zotani, inu anthu achinyengo?

[4] Adzakulangani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo, ndi makala oyaka a mtengo wa tsanya.

[5] Tsoka ine kuti ndimakhala ku Mesaki, kuti ndimakhala pakati pa matenti a ku Kedara!

[6] Kwa nthawi yayitali ndakhala pakati pa iwo amene amadana ndi mtendere.

[7] Ine ndine munthu wamtendere; koma ndikamayankhula, iwo amafuna nkhondo.

Masalimo — Chapters