Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 0:58

[1] Yehova akulamulira, wavala ulemerero; Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu, dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe.

[2] Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale; Inu ndinu wamuyaya.

[3] Nyanja zakweza Inu Yehova, nyanja zakweza mawu ake; nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo.

[4] Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri, ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja, Yehova mmwamba ndi wamphamvu.

[5] Malamulo anu Yehova ndi osasinthika; chiyero chimakongoletsa nyumba yanu mpaka muyaya.

Masalimo — Chapters