Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:22

[1] Patsani mwana wa mfumu nzeru zanu zoweruzira mwa chilungamo, Inu Mulungu mupatseni mwana wa mfumu chilungamo chanu.

[2] Iye adzaweruza anthu anu mwachilungamo, anthu anu ozunzika mosakondera.

[3] Mapiri adzabweretsa chuma kwa anthu anu, timapiri tidzabweretsa zipatso zachilungamo.

[4] Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu ndi kupulumutsa ana a anthu osowa; adzaphwanya ozunza anzawo.

[5] Adzakhala ndi moyo pa mibado yonse, nthawi zonse pamene dzuwa ndi mwezi zikuwala.

[6] Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwa ngati mivumbi yothirira dziko lapansi.

[7] Mʼmasiku a munthu wolungama adzakhazikika; chuma chidzachuluka mpaka mwezi utaleka kuwala.

[8] Iye adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina ndiponso kuchokera ku mtsinje mpaka ku malekezero a dziko lapansi.

[9] Mafuko a mʼchipululu adzawerama pamaso pake ndipo adani ake adzanyambita fumbi.

[10] Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutali adzabweretsa mitulo kwa iye, mafumu a ku Seba ndi Seba adzapereka mphatso kwa iyeyo.

[11] Mafumu onse adzamuweramira ndipo mitundu yonse idzamutumikira.

[12] Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira, wozunzika amene alibe wina womuthandiza.

[13] Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa ndi kupulumutsa osowa ku imfa.

[14] Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawa pakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake.

[15] Iye akhale ndi moyo wautali; golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye. Anthu amupempherere nthawi zonse ndi kumudalitsa tsiku lonse.

[16] Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse; pamwamba pa mapiri pakhale tirigu. Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni; zichuluke ngati udzu wakuthengo

[17] Dzina lake likhazikike kwamuyaya, lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa. Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye ndipo iwo adzamutcha iye wodala.

[18] Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeli amene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa.

[19] Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake. q4 Ameni ndi Ameni.

[20] Uku ndiko kumaliza kwa mapemphero a Davide mwana wa Yese.

Masalimo — Chapters