Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:04

[1] Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera;

[2] Yehova amakonda zipata za Ziyoni kupambana malo onse okhalamo a Yakobo.

[3] Za ulemerero wako zimakambidwa, Iwe mzinda wa Mulungu: q4 Sela

[4] “Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni pakati pa iwo amene amandidziwa. Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi, ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ”

[5] Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti, “Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye, ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.”

[6] Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina: “Uyu anabadwira mʼZiyoni.” q4 Sela

[7] Oyimba ndi ovina omwe adzati, “Akasupe anga onse ali mwa iwe.”

Masalimo — Chapters