Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:13

[1] Onetsani kusalakwa kwanga Inu Mulungu; ndipo mundinenere mlandu wanga kutsutsana ndi mtundu wosapembedza; mundilanditse mʼmanja mwa achinyengo ndi anthu oyipa.

[2] Pajatu Inu Mulungu ndinu mphamvu zanga. Nʼchifukwa chiyani mwandikana ine? Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira, woponderezedwa ndi mdani?

[3] Tumizani kuwunika kwanu ndi choonadi chanu kuti zinditsogolere; mulole kuti zindifikitse ku phiri lanu loyera, kumalo kumene inu mumakhala.

[4] Ndipo ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu, kwa Mulungu, chimwemwe changa ndi chikondwerero changa. Ndidzakutamandani ndi zeze, Inu Mulungu wanga.

[5] Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni iwe moyo wanga? Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandabe Iye, Mpulumutsi wanga ndi Mulungu wanga.

Masalimo — Chapters