Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:09

[1] Inu Mulungu mwatikanatu ife, ndipo mwatiwonongera otiteteza. Inu mwatikwiyira, tsopano tibwezeretseni mwakale!

[2] Inu mwagwedeza dziko ndipo mwalingʼamba, konzani mingʼalu yake pakuti ikugwedezeka kwambiri.

[3] Inu mwaonetsa anthu anu nthawi za mavuto; inu mwatipatsa vinyo amene watichititsa kudzandira.

[4] Koma kwa iwo amene amaopa Inu, Inu mwakweza mbendera kuti tisonkhanireko pothawa uta.

[5] Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja, kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.

[6] Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika: “Mwakupambana ndidzagawa Sekemu ndipo ndidzayeza malire a chigwa cha Sukoti.

[7] Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso; Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera, Yuda ndi ndodo yanga yaufumu

[8] Mowabu ndi mbale yanga yosambira, pa Edomu ndidzaponyapo nsapato yanga, pa Filisitiya ndidzafuwula mwakupambana.”

[9] Adzandifikitse ndani ku mzinda wotetezedwa? Ndani adzanditsogolera ku Edomu?

[10] Kodi si Inu Mulungu, Inu amene mwatikana ife ndipo simutuluka pamodzi ndi magulu athu ankhondo.

[11] Tipatseni chithandizo kuti tilimbane ndi mdani wathu, pakuti thandizo lochokera kwa munthu ndi lopanda phindu.

[12] Chifukwa cha Mulungu, ife tidzapeza chipambano ndipo tidzapondaponda adani athu.

Masalimo — Chapters