Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:30

[1] Inu Yehova, Mulungu amene mumandipulumutsa, usana ndi usiku ndimalira pamaso panu.

[2] Pemphero langa lifike pamaso panu; tcherani khutu lanu kuti mumve kulira kwanga.

[3] Pakuti ndili ndi mavuto ambiri ndipo moyo wanga ukuyandikira ku manda.

[4] Ndikuwerengedwa pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje; ndine munthu wopanda mphamvu.

[5] Ndayikidwa pambali pamodzi ndi anthu akufa, monga ophedwa amene agona mʼmanda, amene Inu simuwakumbukiranso, amene achotsedwa pa chisamaliro chanu.

[6] Mwandiyika pansi pa dzenje penipeni, mʼmalo akuya a mdima waukulu.

[7] Ukali wanu ukundipsinja kwambiri, mwandiopseza kwambiri ndi mafunde anu onse. q4 Sela

[8] Mwandichotsa pakati pa abwenzi anga enieni ndipo mwachititsa kuti ndikhale chonyansa kwa iwo. Ndatsekerezedwa ndipo sindingathe kuthawa;

[9] maso anga ada ndi chisoni. Ndimayitana Inu Yehova tsiku lililonse; ndimakweza manja anga kwa Inu.

[10] Kodi mumaonetsa zozizwitsa zanu kwa anthu akufa? Kodi iwo amene afa amaukanso ndi kutamanda Inu? q4 Sela

[11] Kodi chikondi chanu chimalalikidwa mʼmanda, za kukhulupirika kwanu ku malo a chiwonongeko?

[12] Kodi zozizwitsa zanu zimadziwika ku malo a mdima, kapena ntchito zanu zolungama ku dziko la anthu oyiwalika?

[13] Inu Yehova, Ine ndimalirira thandizo; mmawa mapemphero anga amafika pamaso panu.

[14] Inu Yehova nʼchifukwa chiyani mukundikana ndi kundibisira nkhope yanu?

[15] Kuyambira ubwana wanga ndakhala ndikuzunzika pafupi kufa; ndakhala ndikuchita mantha ndipo ndine wothedwa nzeru.

[16] Ukali wanu wandimiza; zoopsa zanu zandiwononga.

[17] Tsiku lonse zimandizungulira ngati chigumula; zandimiza kwathunthu.

[18] Inu mwatenga anzanga ndi okondedwa anga kuwachotsa pamaso panga; mdima ndiye bwenzi langa lenileni.

Masalimo — Chapters