Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:06

[1] Nʼkwabwino kutamanda Yehova ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba,

[2] Kulengeza chikondi chanu mmawa, ndi kukhulupirika kwanu nthawi ya usiku,

[3] kuyimbira nyimbo choyimbira cha zingwe khumi ndi mayimbidwe abwino a zeze.

[4] Pakuti Inu mumandisangalatsa ndi ntchito zanu, Inu Yehova; Ine ndikuyimba mwachimwemwe pa ntchito ya manja anu.

[5] Ndi yayikuludi ntchito yanu Yehova, maganizo anu ndi ozamadi!

[6] Munthu wopanda nzeru sadziwa, zitsiru sizizindikira,

[7] kuti ngakhale anthu oyipa aphuka ngati udzu ndipo anthu onse ochita zoyipa apindula, adzawonongedwa kwamuyaya.

[8] Koma Inu Yehova, ndinu wokwezedwa kwamuyaya.

[9] Zoonadi adani anu Yehova, zoonadi adani anu adzawonongeka; onse ochita zoyipa adzabalalitsidwa.

[10] Inu mwakweza nyanga yanga ngati nyanga ya njati; mafuta abwino akhuthulidwa pamutu wanga.

[11] Maso anga aona kugonjetsedwa kwa olimbana nane, makutu anga amva za kugwa kwa amaliwongo anga oyipa.

[12] Anthu olungama adzaphuka ngati mtengo wa mgwalangwa, adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni;

[13] odzalidwa mʼnyumba ya Yehova, adzakula bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu.

[14] Iwo adzaberekabe zipatso mu ukalamba wawo, adzakhala anthete ndi obiriwira,

[15] kulengeza kuti, “Yehova ndi wolungama; Iye ndiye Thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe choyipa.”

Masalimo — Chapters