[1] Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse; ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”
[2] Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera ndipo ndidzayamika dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu, pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu kupambana zinthu zonse.
[3] Pamene ndinayitana, munandiyankha; munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.
[4] Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova, pamene amva mawu a pakamwa panu.
[5] Iwo ayimbe za njira za Yehova, pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.
[6] Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa, koma anthu onyada amawadziwira chapatali.
[7] Ngakhale ndiyende pakati pa masautso, mumasunga moyo wanga; mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga, mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.
[8] Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine; chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha musasiye ntchito ya manja anu.