[1] Ife tamva ndi makutu athu, Inu Mulungu; makolo athu atiwuza zimene munachita mʼmasiku awo, masiku akalekalewo.
[2] Ndi dzanja lanu munathamangitsa mitundu ya anthu ena ndi kudzala makolo athu; Inu munakantha mitundu ya anthu, koma makolo athuwo Inu munawapatsa ufulu.
[3] Sanalande dziko ndi lupanga lawo, si mkono wawo umene unawabweretsera chigonjetso, koma ndi dzanja lanu lamanja, mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu, pakuti munawakonda.
[4] Inu ndinu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga amene mumalamulira chigonjetso cha Yakobo.
[5] Kudzera kwa inu ife timabweza adani athu; kudzera mʼdzina lanu timapondereza otiwukirawo.
[6] Sindidalira uta wanga, lupanga langa silindibweretsera chigonjetso;
[7] koma Inu mumatigonjetsera adani athu, mumachititsa manyazi amene amadana nafe.
[8] Timanyadira mwa Mulungu wathu tsiku lonse, ndipo tidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.
[9] Koma tsopano mwatikana ndi kutichepetsa; Inu simupitanso ndi ankhondo athu.
[10] Munachititsa ife kubwerera mʼmbuyo pamaso pa mdani ndipo amene amadana nafe atilanda katundu.
[11] Inu munatipereka kuti tiwonongedwe monga nkhosa ndipo mwatibalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina.
[12] Inu munagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika, osapindulapo kanthu pa malondawo.
[13] Mwachititsa kuti tikhale chochititsa manyazi kwa anthu a mitundu ina, chonyozeka ndi chothetsa nzeru kwa iwo amene atizungulira.
[14] Mwachititsa kuti tikhale onyozeka pakati pa anthu a mitundu ina; anthu amapukusa mitu yawo akationa.
[15] Manyazi anga ali pamaso panga tsiku lonse ndipo nkhope yanga yaphimbidwa ndi manyazi
[16] chifukwa cha mawu otonza a iwo amene amandinyoza ndi kundichita chipongwe, chifukwa cha mdani amene watsimikiza kubwezera.
[17] Zonsezi zinatichitikira ngakhale kuti ifeyo sitinayiwale Inu kapena kuonetsa kusakhulupirika pa pangano lanu.
[18] Mitima yathu sinabwerere mʼmbuyo; mapazi athu sanatayike pa njira yanu.
[19] Koma Inu mwatiphwanya ndi kuchititsa kuti tikhale ozunzidwa ndi ankhandwe ndipo mwatiphimba ndi mdima waukulu.
[20] Tikanayiwala dzina la Mulungu wathu kapena kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo,
[21] kodi Mulungu wathu sakanazidziwa zimenezi, pakuti Iye amadziwa zinsinsi zamumtima?
[22] Komabe chifukwa cha Inu timakumana ndi imfa tsiku lonse, tili ngati nkhosa zoyenera kuti ziphedwe.
[23] Dzukani Ambuye! Nʼchifukwa chiyani mukugona! Dziwutseni nokha! Musatikane kwamuyaya.
[24] Nʼchifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu, ndi kuyiwala mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu?
[25] Tatsitsidwa pansi mpaka pa fumbi; matupi athu amatirira pa dothi.
[26] Imirirani ndi kutithandiza, tiwomboleni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.