[1] Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira ndi zoyipa, iwe munthu wamphamvu? Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira tsiku lonse, iwe munthu wochititsa manyazi pamaso pa Mulungu?
[2] Tsiku lonse umakhalira kuganizira za kuwononga ena; lilime lako lili ngati lumo lakuthwa, ntchito yako nʼkunyenga.
[3] Iwe umakonda choyipa mʼmalo mwa kuyankhula choonadi. Umakonda kunama kupambana kuyankhula zoona. q4 Sela
[4] Umakonda mawu onse opweteka, iwe lilime lachinyengo!
[5] Zoonadi Mulungu adzakutsitsa kupita ku chiwonongeko chamuyaya: iye adzakukwatula ndi kukuchotsa mʼtenti yako; iye adzakuzula kuchoka mʼdziko la amoyo.
[6] Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha; adzamuseka nʼkumanena kuti,
[7] “Pano tsopano pali munthu amene sanayese Mulungu linga lake, koma anakhulupirira chuma chake chambiri nalimbika kuchita zoyipa!”
[8] Koma ine ndili ngati mtengo wa olivi wobiriwira bwino mʼnyumba ya Mulungu; ndimadalira chikondi chosatha cha Mulungu kwa nthawi za nthawi.
[9] Ine ndidzakutamandani kwamuyaya chifukwa cha zimene mwachita; chifukwa cha zimene mwachita; mʼdzina lanu ndidzayembekezera pakuti dzina lanulo ndi labwino. Ndidzakutamandani pamaso pa oyera mtima anu.